Friday, July 27, 2007

YESU CIPULUMUTSO!

Chewa


J.D. Phillips

1. KHULUPIRIRA Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka a m’banja mwako. (Ntchito 16:31) Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. (Aheberi 11:5) Koma yemwe sadzakhulupirira, Mulungu adzamlanga. (Marko 16:16) Pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine amene ndili,,udzaferadi m’machimo anu. (Yohane 8:24) Koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino, nchakufa. (Yakobo 2:17).

2. LAPANI, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Kristu.(Ntchito 2:38) Koma ngati simulapa, inunso mudzwonongedwa nonga iwo aja. (Luka 13:3,5) Mulungu ... koma tsopano aliku;amula anthu onse ponseponse kuti alape. (Ntchito 17:30) Motero Mulungu wapatsa anthu a nitundu yina omwe mwayi woti alapedi kulandira moyo! (Ntchito 11:18)

3. Ngati ubvomereza pakamwa pako kuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo ngati ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamulitsa kea akufa, udzapulumuka.(ARoma 10:9) Aliyense wondibvomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzambvomereza pamaso pa Atate anga a Kumwamba. (Mateo 10:32) Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wampyo. (Mateo 16:16) Ndikhulupirira kuti Yesu Kristu ndiye Mwana wa Mulungu. (Ntchito 8:37)

4. UBATIZO umene lero ukupuhumutsani (I Petro 3:21) Yemwe akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, (Marko 16:16) Zoonadi ndikukuuza kuti ngati munthunsabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera,sangathe kulowa mu Ufumu wa Mulungo. (Yohane 3:5) Anatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano. (Tito 3:5) Lapani, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m’dzina Ia Jesu Kristu. (Ntchito 2:38) Dzuka, ndipo petamando dzina lake, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke. (Ntchito 22:16) ndi Kristu pakubatizidwa, (AmaGalatia 3:27) Kodi simudziwa kuti tonse amene tinasanduka amodzi ndi Kristu Yesu pakubaptizidwa, ndi ubatizo womwewo tinasandukanso amodzi ndi Iye muimfa yake? (Aroma 6:3) Ngati munthu ali mwa Kristu, ngolengedwa kwatsopano. (2 Akorinto 5:17)

5. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kuti tisiye moyo wosachitira Mulungu ulemu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodzi;etsa, wolungama ndiponso wochitira Mulungu ulemu. Pakuti tilikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tilikuyembekeza, ndipo tidzaona Mulungu wammkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu alikubwera mwaulemerero. Iyeyu anadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse kuzoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pantchito zonse zabwino. (Tito 2:12-14)

Ndipo kuti mumasunga chiphunzitso chimene ndinakusiyirani. (1 Akorinto 11:2)

Ambuye Yesu akudalitseni nonse. (Chibvumbulutso 22:21)

Ngodala amene achapa mikanjo yawo, kuti aloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyo, ndiponso kulowa mumzinda kudzera pazipata zija. (Chibvumbulutso 22:14)

No comments: